KONDOWE WASEWERA MWAPAMWAMBA MU AUGUST KU BULLETS
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, wasankhidwa kukhala osewera yemwe wasewera bwino kuposa onse kutimuyi mu mwezi wa August pomwe walandira mavoti ochuluka kuchokera kwa ochemerera atimuyi.
Kondowe wagonjetsa wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa komanso wapakati, Chawanangwa Gumbo pa mavoti kuti atenge mphotoyi kamba kopulumutsa Bullets kangapo mu mwezi umenewu.
Iye wagoletsa zigoli zitatu mu mweziwu zomwe zinali zofunikira kwambiri kutimuyi ndipo mmasewero onse omwe wasewera mu mweziwu, onse amachokera panja.
Iye alandira kachikho kakang'ono ndi ndalama yokwana K100,000 kuchokera ku kampani ya Hubertus Clausius Insurance kamba kopambana mphotoyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores