"CIVO ITHERA MU TOP 8" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Oscar Kaunda, wati timu yake ithera mkatikati mwa matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi ya TNM angakhale kuti sakuchita bwino mmasewero awo.
Kaunda amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Blue Eagles pa bwalo la Champions ku Dowa. Iye wati timu yake ikuphonya mipata yambiri koma akonza mavutowa.
"Tikupeza mipata yochuluka koma tikukanika kuipanga zigoli tingobwerera kuti tikakonze ndipo tithera mu top 8. Anthu ankakaika mu chigawo choyamba chija koma tinathera pa nambala 7, apapanso tipanga zinthu." Anafotokoza Kaunda.
Timu ya Civo ili ndi point imodzi pamwamba pa malo opulumuka pomwe ili ndi mapointsi 24 pa masewero makumi awiri ndi amodzi (21) mu ligi ya chaka chino.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores