"MPHECHEPECHE MWA NJOBVU SAPITAMO KAWIRI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati sakufunanso kuti timu yake ibwererenso kumunsi kwa ligi komwe iwo anali kamba koti mmene ligi yavutiramu palibe timu yomwe ili pa mtendere.
Nyambose amayankhula izi timu yake itafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) kutsatira kugonjetsa Red Lions 1-0 pa bwalo la Kamuzu. Iye anati timu yake sinasewere bwino koma zilibe ntchito pomwe pakadali pano chipambano nde chofunikira.
"Tiyesetsabe kuti tipitilize kupeza zipambanozi chifukwa mphechepeche mwa njobvu sapitamo kawiri, kumunsi kuja sitikufuna tibwererenso nde tiyesetsa kupambana mmasewero athu." anatero Nyambose.
Tigers yatsala ndi masewero asanu ndi atatu (8) kuti imalize ligi ya chaka chino ndipo yakwanitsa kutolera mapointsi 27 ndipo ali ndi mapointsi anayi pamwamba pa malo amatimu otuluka mu ligi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores