KARONGA YAKONZEKA KUPHA KB
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake yakonzekera bwino patsogolo pa masewero awo ndi Kamuzu Barracks omwe achitike pa bwalo la Kasungu loweruka.
Kajawa wati timu yake yayenda bwino kuchoka ku Karonga ndipo tsopano maso awo akuyang'ana pa masewero awo ndi KB omwe akufunikira chipambano.
"Akhala masewero ovuta poti KB nayonso ndi timu yabwino koma anyamata akudziwa kufunikira kwa kupambana masewerowa nde pakadali pano anyamata akutsogolo tili nawo abwino kwambiri ndipo zigoli zizipezeka. Anthu abwere ndipo adzaonera mpira wabwino." Anatero Kajawa.
Karonga ikuchokera kogonjetsa timu ya Ekwendeni Hammers 4-1 ndipo ili pa nambala 11 mu ligi ya TNM ndi mapointsi 21 pa masewero 18 yomwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores