"TIGERS IKUTIPEZA MU NYENGO YOWAWA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake ndiyokonzeka kuti asewere ndi Mighty Wakawaka Tigers ndipo ayesetsa kulimbikira kuti apambane pomwe ali ndi mu nyengo yowawa.
Kananji amayankhula izi patsogolo pa masewero awowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zokonzekera zokhudza masewerowa zayenda bwino.
Iye wati padakali pano anyamata onse omwe anali ovulala ali bwino tsopano ndipi zingotengera kuti abwera motani kuchokera kuvulalako. Iye watinso ndi okondwa kamba ka zokambirana zomwe zinalipo mkati mwa sabatayi zomwe zithandize kuchitanso bwino kwa timu.
Eagles ili pa nambala 15 mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi 17 pa masewero 18 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores