ADELEKE WACHIRA KU NOMA
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Adeleke Kolawole, tsopano wachira ndipo atha kuyambapo kuoneka pa bwalo la zamasewero pomwe tsopano wayamba zokonzekera ndi timu yonse.
Katswiriyu anafika mdziko muno mwezi watha atabwereranso pomwe Wanderers inakondabe ntchito zake angakhale kuti anali pa ndandanda wa osewera omwe anachotsedwa chaka chatha.
Iye anabwera atavulala koma tsopano katswiriyu ali bwino ndipo atha kupezeka pa masewero atimuyi ndi MAFCO lamulungu likudzali.
Katswiriyu anabwera ku Wanderers chaka Chatha pomwe anamugula kuchokera ku timu ya Karonga United.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores