"ZA KAMPANI YATSOPANO SINDIKUZIDZIWA" - MPINGANJIRA
Mkulu wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Roosevelt Mpinganjira, wati zoti ku timuyi kukubwera kampani yoti izithandiza ku ntchito Ina sakuzidziwa.
Mpinganjira wayankhula izi mmawa wa lachinayi pomwe anafunsidwa malingana ndi malipoti omwe masamba ena olemba nkhani analemba lachitatu kuti kampani ina ikubwera kuti izithandiza timuyi.
"Zimenezo sindikudziwa, sindingathe kutsutsa ndithu koma ndati sindikudziwa ine." Anatero Mpinganjira pomwe amayankhula ndi Wayilesi ya Ndirande FM.
Timu ya Wanderers ili ndi makampani angapo monga Mukuru, Ekhaya Foods ndi a Smile life Insurance omwe amathandiza mu ntchito za timuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores