MALAMULO OMWE MALAWI YASAINA AKHUDZA BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikhonza kuluza omwe amawathandiza a Nyasa Manufacturing company pomwe malamulo a World Health Organization ochepetsa mulingo wa Fodya akukaniza kampani yopanga Fodya kuthandiza masewero a mpira.
Dziko la Malawi lalowa mu mgwirizanowu pa 18 August ndipo yakhala dziko la nambala 183 kutenga malamulowa omwe amachepetsa kapangidwe komanso kasutidwe ka Fodya.
Zina mwa malamulo omwe ali mu mgwirizanowu ndi oletsa kulengezetsa kwa malonda a Fodya mwa njira Ina iliyonse komanso thandizo lopita ku matimu kapena zikho zaku mpira wa miyendo.
Zateremu, Malawi itengera malamulowa ndipo timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi imene ikhudzidwe poti ndi imene imathandizidwa ndi imodzi mwa makampani opanda ndudu. Nyasa yakhala ikuthandiza Bullets kuchokera mu 2015.
Source: Nation
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores