BLUE EAGLES YALONJEZA KUBWERERANSO KWA CHIPAMBANO
Timu ya Blue Eagles yati zokambirana zomwe apanga kutimuyi lachitatu zofuna kukonza kuti timuyi iyambenso kuchita bwino zinali zofunika ndipo timuyi iyambiranso kuchita bwino.
Wapampando watimuyi, Alex Simenti, wati sangakambe zambiri pa zomwe anakambirana pa mkumanowu koma wati mbali zonse zafotokoza mavuto awo ndipo zonse zitha.
"Titaona mavuto aja tinaona kuti ndi kwabwino kuitana mbali zonse zokhudziwa kuti tikambirane ndipo aliyense wakamba mavutowa, mmasewero omwe akubwerawa tiwina ndithu." Simenti anafotokoza.
Mu mkumano womwe unatenga maola asanu ndi likulu la timuyi, unakhudza wachiwiri kwa wamkulu wa apolisi mdziko muno, akuluakulu ena, aphunzitsi, osewera komanso ochemerera kutimuyi omwe amafotokoza nkhawa zawo ndi kuzikonza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores