EAGLES YAITANITSA MKUMANO
Timu ya Blue Eagles ikhale ndi mkumano wa akuluakulu a timuyi, osewera komanso aphunzitsi lachitatu pomwe akufuna akawunikire chifukwa chimene timuyi isakuchita bwino.
Izi zikutsatira pempho la mphunzitsi watimuyi, Eliya Kananji, lopita kwa akuluakulu atimuyi kutsatira kugonja 1-0 ndi Moyale Barracks pakhomo pawo sabata yatha.
Mkumano omwe wakonzedwawu ukhudzanso wapampando wakale wa timuyi, Alexander Ngwala, omwe ayitanidwa kuti akamvetse mavuto omwe ali kutimuyi.
Eagles ili pa nambala yachiwiri kuchokera kumunsi ndi mapointsi 17 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores