BULLETS IFIKA LERO
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ifika mdziko muno lero pomwe ikuchokera mdziko la Equatorial Guinea komwe yakaphodorako timu ya Dragon FC mu mpikisano wa CAF Champions league.
Mkulu oyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati timuyi ifika masana wa pa bwalo la Chileka mu mzinda wa Blantyre.
Iye watinso matikiti amasewero achibwereza omwe adzachitikire pa bwalo la Bingu lamulungu likudzali ayamba kale kugulitsidwa ndipo wati ali pa mtengo wa K2,000.
Iye wapempha amalawi kuti akasapotere timuyi ndi cholinga choti akagonjetse Dragon poti masewerowa akadali onse ndipo sanathe. Maxwell Gasten Phodo ndi yemwe anagoletsa zigoli ziwiri ku Malabo kuti Bullets ipambane 2-0.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores