"TIKUFUNA KUTHERA MU MATIMU ASANU OYAMBA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watsopano watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati wauza osewera ake kuti akufuna timuyi ithere mu matimu asanu oyambilira mu ligi ya TNM chaka chino ikamadzatha.
Mkandawire amayankhula izi pomwe timuyi inagonjetsa Silver Strikers 3-2 pa bwalo la Kamuzu ndipo iye anati anali okhutira ndi mmene anyamata ake anasewerera.
Iye wati wauza anyamata ake kuti asagone chifukwa akufunitsitsa atamaliza kumtunda kwa ligi.
"Masomphenya anga ndaika kuti tithere mu top 5, ndawauza kale anyamatawa ndipo ndi zotheka." Anatero Abel Mkandawire.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndipo akuchepekedwa ndi point imodzi kuti afike pa nambala yachisanu mu ligiyi yomwe pali timu ya Kamuzu Barracks.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores