WAPOLISI ANAKWENYEDWA NDI OYIMBIRA
Malipoti akusonyeza kuti oyimbira pa masewero a pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Blue Eagles, Mayamiko Kanjere anakwenya osewera wa timu ya Blue Eagles, Micium Mhone, osewerayu atamuputa posamuyankhula mawu abwino.
Izi zadza pomwe wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale anadandaula kuti timu yake inagonja masewero chifukwa oyimbira anaopseza osewera atimuyi. Koma limodzi mwa masamba olemba nkhani dziko muno, Wa ganyu, linafuna kufunsa Kanjere koma anakana kuyankhulapo.
Koma mmodzi mwa omwe amapereka chitetezo pamasewerowa anauza tsambali kuti Mhone ndiyemwe anayambitsa.
“Micium adalankhula mawu amene sadasangalatse Kanjere ndipo iye anati kuopsezedwa sikumagwira kwa iye. Adati ine ndekha ndimamenya ndiye iyiyi ndi ya iweyo ndi ineyo tithane. Adati iyiyi siyopatsananso makadi koma iwe ndi ine nde Mu tunnel mujatu ndiye ref adamukwenya Micium mpaka tidaleretsa.” Iye anatero.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores