WANDERERS NDI CHITIPA KACHIKENANSO
Matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Chitipa United ndi omwe ayikidwa kuti adzakumane pa mwambo okumbukira tsiku lomwe dziko lino linatenga ufulu ozilamulira tokha, pa 06 July, ku bwalo la Bingu.
Mmodzi mwa atolankhani athu, auzidwa ndi osewera wina wa Chitipa yemwe anati asatchulidwe dzina koma anati ndi chilimbikitso kwa iwo monga timu yaying'ono kukasewera masewero ngati amenewa.
Matimuwa anakumanapo mu TNM Supa ligi pa bwalo la Kamuzu ndipo Chitipa inapambana 1-0 ndi chigoli cha Miracle Gabeya chodzimwetsa yekha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores