Timu ya osewera mpira wa miyendo ya amayi ya dziko la South Africa - Banyana Banyana ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Malawi Scorchers pa masewero a paubale omwe achitike pa 5 ndi 8 April m'dziko la South Africa.
Izi zadziwika pomwe mphunzitsi wa timu ya dzikoli, Desiree Eliis amatulutsa ndandanda wa atsikana omwe atumikire mu masewero opimana mphamvuwa ndipo watenga osewera okwana makumi awiri ndi atatu (23).
Timu ya Banyana Banyana ikuyembekezeka kuzakhala ndi osewera awo onse omwe amadalira monga Linda MOTLHALO yemwe amasewera ku Scotland mu team ya Glasgow Rangers komanso Thembi KGATLANA.
Zikomo kwambili
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores