"PENA TIMAKANIKA KUWINA CHIFUKWA CHA ANTHU ENA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati sanasangalale ndi zotsatira pa masewero kamba koti oyimbira wawakanira chigoli chabwinobwino nthawi yothaitha.
Makawa amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Chitowe ndipo wati angakhale timu itasewera bwino, zinthu zina zimalepheretsa kuti apambane.
"Sindinakhutire ndi zotsatirazi tinasewera bwino tinapeza zigoli ziwiri, Iwo anabwenza ndi chigoli chopatsidwa chabwino koma tagoletsa china oyimbira achikana chabwinobwino nde masewero ena titha kusewera bwino koma ena amatikaniza kupambana." Anatero Makawa.
Iye wati anthu ayembekezere kuti timuyi itola mapointsi ochuluka kuposa omwe atola mchigawo choyamba poti tsopano anyamata ake ayamba kugwirana.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi 20 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi.
π·: Civo media
Pena oyimbila athu ndichifukwa sakupasidwira mpata okayimbila mipikisano yikuluyikulu kunjaku chifukwa chamagwiridwire ntchito awo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores