Bungwe la Confederation of African Football (CAF) laletsa Ivory Coast kugwiritsa ntchito mabwalo a mdzikolo ponena kuti sakufikira mlingo yoyenera.
CAF yanena izi m'chikalata chomwe atulutsa pambuyo pa masewero a timu ya Ivory Coast ndi Cameroon omwe anachitikira mdzikolo.
Malingana ndi bungwe la CAF, Ivory Coast ikuyenera kusankha bwalo lomwe agwilitse ntchito masewero otsatira m'maiko ena.
Padakali pano masewero apakhomo a timu ya Mozambique omwe isewere ndi Malawi komanso Cameroon achitikira ku Morocco.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores