BAKA IKUTOLERA MAPOINTSI ITATULUKA
Mapointsi omwe amavuta kupezeka kutimu ya Baka City isanatsimikizike kuti yatuluka mu ligi ayamba kupezeka tsopano atatuluka mu ligi pomwe yakwanitsa kutolera mapointsi anayi pa masewero awo awiri apitawa.
Timuyi inakanika kupeza chipambano chawo chachitatu mu ligi pomwe inabwenzetsa zigoli ziwiri kuti ilepherane 2-2 ndi timu ya Mighty Tigers pa bwalo la Karonga masana a loweruka.
Tambulani Mwale anatsogoza timuyi mchigawo choyamba asanathandizire chigoli cha Edgar Phiri mchigawo chachiwiri koma Kelvin Nyondo anazigoletsa yekha Precious Chipungu asanabwenze kuti agawane point imodzi imodzi.
Mphunzitsi wa magoloboyi kutimuyi, Davie Kayira, anati timu yake inakanika kutchinga bwino kumbuyo kwawo kupangitsa kuti abwenzetse zigoli koma iwo sikuti akuphwekanso kuti aziluza.
"Tikungosewera poti basi tinafa kale koma sizikutanthauza kuti basi tizingoluza ayi. Tizisewera ndithu bola tizifananitsa mphamvu chonchi osati kugonja ayi." Anatero Kayira.
Tumizilani ku 0981511741
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores