"ANYAMATA AMAONA NGATI APAMBANA KALE" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC Enos Chatama wati kaganizidwe ka osewera ake kachititsa kuti akanike kugonjetsa Goshen City Dedza Dynamos pomwe wati anawaderera masewerowa asanayambe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 pa bwalo la Mpira pomwe Blessings Malinda anagoletsa Ekhaya ndipo Marcos Chiwaya anamwetsa kumbali ya Dynamos.
Chatama wati osewera ake ayamba kumadelera masewero omwe akumaoneka ngati aang'ono zomwe zikufunika kusintha ndi cholinga choti azitha kupeza mapoints ambiri.
"Masewero akuluakulu aja tinachita bwino nde anyamata anazolowera kuti mwina awa ochepera mphamvuwa azipambana mophweka zomwe zikuyenera kuchoka kaganizidwe kameneka," anatero Chatama.
Iye anatinso timu yakeyi inaphonya mipata yochuluka komanso kuti masewerowa akanapambana mophweka koma osewera anawachepetsa kwambiri angakhale nthawi yomwe amatsogola.
Timuyi yafika pa nambala yachisanu pomwe ili ndi mapoints 17 pa masewero 12. Timuyi ya
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores