"WANDERERS NDI BLUE EAGLES TILI NAWO NTCHITO YAPADERA" - CHIMKWITA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United Christopher Chimkwita wati nthawi yakwana yoti osewera ake azipangire mayina pomwe wati anayika masomphenya oti afike mu ndime yotsiriza ya Airtel Top 8 komwe alinso ndi mangawa ndi Mighty Wanderers komanso Blue Eagles.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Ekhaya FC omwe aliko loweruka pa bwalo la Silver ndipotu wati zonse zoyenera kuchita osewera ake awuzidwa kwatsala ndi kukagwira ntchito.
"Tasewerapo pa Silver kangapo koma sizikutipatsa mwayi kuti tidzachita bwino ayi, tikukumana ndi timu yabwino kwambiri yomwe zawo zambiri zimayenda komabe ifeyo tikukagwira ntchito," anatero Chimkwita.
Iye wati masomphenya awo anayika pogonjetsa Silver Strikers yomwe imawavuta kwambiri ndipo kenako kufika mu ndime yotsiriza ndilo khumbo lawo komwe akakumane ndi Blue Eagles kapena Wanderers omwe ali nawo mangawa.
Karonga inafikapi mu ndime yotsiriza ya chikhochi mu 2019 komabe inagonj
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores