EKHAYA YAKONZEKA KUKUMANA NDI KARONGA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC Enos Chatama wati osewera atimu yake akufunitsitsa atasewerako mu ndime yotsiriza ya chikho cha Airtel Top 8 ndipo ndi wokonzeka pa masewero awo amu ndime ya matimu anayi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Karonga United loweruka pa bwalo la Silver ndipo wati akudziwa kuti ali ndi timu yabwino kwambiri yomwe imugwilire ntchito.
"Masewero amu chikho amakhala ovuta pomwe timu yodelelekayo ndi yomwe imatha kukugonjetsani komabe anyamata ndi timu okonzeka kuti adzachite bwino," anatero Chatama.
Iye wati akudziwanso kuti Karonga ili ndi mbiri yabwino mu mpikisanowu koma sakuchita mantha kamba koti FCB Nyasa Big Bullets yomwe iwonso anayitulutsa inali ndi mbiri yabwinonso mu chikhochi.
Ndipo mtsogoleri wa osewera atimuyi Clever Nkungula wati osewera onse ndi okonzeka bwino pa masewerowa.
"Awa ndi masewero ovuta kwambiri komabe anyamata akudziwa kufunikira kwa masewerowa ndi ntchito yomwe ili patsogolo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores