"IFENSO TILI NDI ZIDA ZOTI TITHA KUKAYIDZIDZIMUTSA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers Lovemore Fazili wati alibe mantha chifukwa choti Nigeria sinagonjeko kwa zaka ziwiri ndipo ayika chidwi pa zofooka za anzawowo kuti akathe kuwagonjetsa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Nigeria lachiwiri mu mpikisano wa Women's African Cup of Nations.
Iye wati akudziwa kufunikira kwa masewerowa ndipo ngati mmbuyomu sizimayenda, uku ndi kumpikisano kumene akhale akuyikapo mtima kwambiri.
"Ndili ndi chikhulupiliro kwambiri ndi osewera omwe tigwiritse ntchito. Ndikudziwa nawo ndi timu yabwino komabe ifenso tili ndi zida zomwe akadzangophetira pang'ono tidzawadzidzimutsa. Tayang'ana kwambiri pa zofooka zawo kuti tidzawalowere pamenepo," anatero.
Aka kakhala koyamba kuti Malawi isewere mu mpikisanowu ndipo Fazili wati aonetsa kuti Malawi sinangopita ku mpikisanowu mwa tsoka.
Nigeria ndi timu imene ikuteteza ukatswiri wa chikhochi ndipo yatengako ka khumi. Matimu ena omwe ali mu gul
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores