"TIYESETSA KUTI TICHITE BWINO PAKHOMO" - MPINGANJIRA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers Bob Mpinganjira wati ndi zopambana kuti timuyi ikumatha kupezeka pamwamba pa ligi ya FDH Premiership koma sakufuna kuwapatsa phuma anyamata ake pa masewero omwe akumasewera.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Masters FC omwe aliko lamulungu pa bwalo la Mpira mu mzinda wa Blantyre.
Mpinganjira wati timu yake ndi yokonzeka kwambiri mu masewerowa ndipo akuyenera kugwilitsa ntchito mwayi wosewerera pakhomo mu masewerowa.
"Akhala masewero ovuta chifukwa tikukumana ndi timu yabwino koma anyamata ndi okonzeka ndipo akudziwa kufunikira koti tipambane masewerowa," anatero Mpinganjira.
Iye watsimikiza kuti Alex Kambirinya apezeka pa masewerowa pomwe anapita ku Super League of Malawi kukaonetsa kadi kuonetsa kuti ndi wovomerezeka kusewera.
Iye watinso Emmanuel Nyirenda wachira chimodzimodzinso Isaac Kaliati yemwe ayambe zokonzekera sabata ya mawa koma Blessings Mwalilino ndi Chimwemwe
Blessings Mwalilino ndi Chimwemwe Nkhoma kukadalibe.
Manoma alowa mu masewerowa ali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ali ndi mapoints 21 pa masewero khumi omwe asewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores