"TIVOMEREZE KUTI LERO TAGONJA" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC Enos Chatama wati timu yake inali ndi zinthu zingapo zomwe sanachite bwino pa masewero awo zomwe zawachititsa kuti agonje koma akakonza chifukwa masewero ndi ochuluka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Chitipa United ndi chigoli cha Chancy Kaonga mu chigawo chachiwiri pa bwalo la Chitipa loweruka masana.
Chatama wati mmbali mwawo mumakanika kuyenda kwambiri komanso kuti anakanika kumenyera pagolo zomwe zawachititsa kuti asachite bwino konse pa masewerowa.
"Zimachitiks mu mpira kugonja, tasewera masewero asanu ndi amodzi osagonja koma lero tagonja tivomereze tibwerera tikakonze ziwiri zitatu zomwe taona kuti zativuta," anatero Chatama.
Iye anati chipambano chikanakhala chofunikira kwambiri koma tsopano ayika chidwi pa masewero omwe atsala nawo kuti adzachite bwino.
Timuyi ikadali pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapoints 16 pa masewero 11 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores