AKIDU WAPAMBANA MPHOTO YA MPHUNZITSI WAPAMWAMBA MU MAY
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekhaya Fundi Akidu wapambana mphoto ya mphunzitsi wapamwamba mu mwezi wa May kutsatira kuchita bwino pomwe ankagwirizira pa ntchito yauphunzitsi kutimuyi.
Izi zadziwika pomwe bungwe la Super League of Malawi latulutsa zotsatira za mphotoyi yomwe anatulutsa mayina omwe akupikisana masabata atatu apitawa.
Akidu anatsogolera Ekhaya kupambana masewero atatu ndi kugonja amodzi pa nthawi imene mphunzitsi wamkulu Enos Chatama anali ku tchuthi.
Iye wagonjetsa mphunzitsi wa Blue Eagles De Kleck Msakakuona komanso Peter Mponda wa Masters FC kuti atenge mphotoyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores