"ANYAMATA ANADZIDZIMUKA CHIFUKWA ANAZOLOWERA KUCHITA BWINO" - NYEMERA
Mphunzitsi watimu ya Goshen City Dedza Dynamos Lazarus Deco Nyemera wati anyamata ake anakanika kuti abwerere mu masewero atachinyitsa chigoli choyamba kamba koti anazolowera kusachinyitsa ndi kupambana zomwe zinawadzidzimutsa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi Chitipa United pakhomo ndipo wati momwe anakonzera kuti asewere sizinagwire ndi momwe anzawo anasewerera.
"Tinakonza kuti mwina tichinye mwachangu komatu anzathu anaoneka kuti akonzeka kwambiri nde tinachinyitsa zomwe zinatidzidzimutsa kwambiri ndipo tinavutika kuti tibweremo," anatero Nyemera.
Iye watinso kugonjako kwawabwenzeretsa mmbuyo kamba koti amafunitsitsa kusuntha pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Kutsatira kugonjaku, timuyi ili pa nambala 14 mu ligi ndi mapoints asanu ndi atatu pa masewero khumi omwe asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores