"TIPITA MMASEWEROWA KUTI TIKAPAMBANE" - MPINGANJIRA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers Bob Mpinganjira wati timu yake ikupita ku Lilongwe ndi cholinga chimodzi chokha kuti apeze chipambano ndi kuziyika pabwino pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero atimuyi ndi Civil Service United pa bwalo la Civo loweruka masana.
Iye wati akudziwa Kuti masewerowa akhala ovuta chifukwa choti Civil imavuta pakwawo koma akayesetsa kuti akachite bwino mu masewerowa.
"Tikasewera masewerowa mopanda phuma lililonse kuti tichinye tichinye koma chomwe tikayang'ane ndi kuti tipambane tipite patsogolo pa ndandanda wa matimu mu ligi," anatero Mpinganjira.
Iye watinso osewera monga Isaac Kaliati ndi Jacob Anyandwile sapezeka kamba ka kuvulala komanso kudwala ndipo ali mu gulu la Emmanuel Nyirenda, Blessings Mwalilino ndi Chimwemwe Nkhoma.
Wanderers ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapoints 18 pa masewero asanu ndi anayi omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores