MITHI NDI SINGINI ACHIRA
Timu ya Mighty Wanderers ikhala ndi osewera awo odalilika Blessings Singini komanso Lameck Mithi pa masewero omwe akumane ndi Creck Sporting Club mu masewero achibwereza amu chikho cha Airtel Top 8 mu ndime ya matimu asanu ndi atatu.
Izi zadziwika pomwe mphunzitsi watimuyi Bob Mpinganjira amatsimikiza za osewera omwe wayenda nawo patsogolo pa masewerowa ku bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji lamulungu.
Iye wati awiriwa tsopano achira ndipo apanga nawo zokonzekera ndi timuyi.
"Emmanuel Nyirenda yekha ndi yemwe akadali wovulala chimodzimodzinso Chancy Mtete ndi Blessings Mwalilino omwe avulalanso ndipo akuunikidwa ndi ma dotolo," anatero Mpinganjira.
Iye watinso timuyi sikupita mophweketsa Creck chifukwa imavutika Kuti ipambane ndi timuyi ndipo akayesetsa kuti apeze zigoli zochuluka kuti afike mu ndime ya matimu anayi yamu chikhochi.
Wanderers ikupita mu masewerowa ikutsogola 2-0 kutengera ndi zigoli zomwe anagoletsa mu masewero oyamba mwezi watha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores