Bungwe loyendetsa ligi yaikulu mdziko muno la Super League of Malawi lalengeza kusintha kwa bwalo lomwe lichititse masewero a FCB Nyasa Big Bullets ndi Masters FC kuchoka pa bwalo la Mpira kupita ku Joyce Chitsulo ku Mwanza.
Bungweli lalengeza za nkhaniyi lachiwiri masana pachifukwa choti bwaloli lidzakhala likugwiritsidwa ntchito zina.
Ndipo mu kusintha kwina, masewero a Silver Strikers ndi Red Lions omwe amayenera kuseweredwa loweruka asunthidwa kufikira lamulungu kamba kotinso bwalo la Silver lidzakhala lotangwanika patsikuli.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikanasewera masewero awo oyamba pa bwalo la Mpira Chaka chino ngati pakhomo kutsatira kuti timuyi ikumavutika ku Mwanza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores