DEDZA YACHAPIDWA KU CHITOWE
Zinthu zikupitilira kuyipirabe kutimu ya Goshen City Dedza Dynamos pomwe yagonja 3-0 ndi timu ya MAFCO pa masewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Chitowe ku Nkhotakota loweruka masana.
Timu ya MAFCO inapeza zigoli zawo kuchokera kwa Zikani Sichinga mchigawo choyamba ndipo Blessings Mofolo anamwetsa ziwiri mchigawo chachiwiri kuti apeze chipambanochi.
Dynamos inali ikuchokera kopeza chipambano chawo choyamba ndipo imakhulupilira kuti ipitira kuchita bwino koma sizinatero.
Mphunzitsi watimuyi Alex Ngwira wati timu yake ikuchinyitsa zigoli mophweka komanso kuphonya mipata mu masewero awo.
"Ifeyo ndi omwe tinali ndi mipata koyambilira koma tinaphonya nde zikatere anzanu amakuwerengani tachinyitsa zigoli zophweka, tinapezanso penate yomwe sinamenyedwe mwa nzeru bwinobwino," anatero Ngwira.
Iye anatinso osewera ambiri omwe ali nawo ndi achisodzera ndipo akadaphunzira pang'onopang'ono.
Dynamos ikadali pa nambala 15 ndi mapoints anayi pa masewero asanu ndi awi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores