Anthu okonda masewero akuyenera kupisa mthumba molowa mmanja ngati akufuna kudzaonera masewero a Mighty Wanderers ndi Ekhaya FC kamba koti ayikidwa pa K10,000 ku malo okhalako adzuwa.
Izi ndi malingana ndi mitengo yomwe eni khomo omwe ndi a Wanderers omwe akuti kumalo otchinga ndi K15,000.
Komabe masapota a timuyi adandaula ndi mtengowu kamba koti mitengo yomwe anatulutsa a bungwe la Super League of Malawi inathera pa K7,000.
Matimu a Mighty Wanderers ndi Ekhaya akumana loweruka pa bwalo la Mpira mu Sabata yachisanu ndi chiwiri yamu ligi ya FDH Premiership.
📷 MH photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores