"TAPHONYA KWAMBIRI MIPATA YATHU KOMA TIKONZA" - MUNTHALI
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati siokhutira ndi kaseweredwe katimuyi mu chigawo chachiwiri cha masewero awo ndi timu ya Ekhaya ponena kuti amataya mipira yochuluka komanso kumangobwenza mipira kumbuyo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi Ekhaya mu ndime ya matimu asanu ndi atatu amu chikho cha Airtel Top 8 pa bwalo la Bingu loweruka.
Munthali wati timu yake imayenera kuteteza chigoli chawo chomwe anachipeza mu mphindi zoyamba za chigawo chachiwiri ndipo akonza mavuto awo.
"Mchigawo choyamba tinapeza mipata yomwe timayenera kugoletsa koma tinalephera, titawauza mchigawo chachiwiri tinapeza chigoli koma sitinasewere bwino," iye anatero.
Iye anatinso akudziwa kuti azipatsa ntchito yochuluka yoti akagwire mu masewero achibwereza koma akonza zonse kuti adzachite bwino mmasewerowa.
Timuyi idzakhala pakhomo mu masewero achibwereza pa bwalo la Mpira mu mzinda wa Blant
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores