RED LIONS YALOZA CHALA OYIMBIRA ITAGONJA KOYAMBA
Timu ya Red Lions yaloza chala oyimbira pa masewero awo ndi Karonga United kuti wawaonongera masewero kupangitsa kuti agonje koyamba mu ligi ya FDH Premiership.
Mphunzitsi watimuyi, Malumbo Mkandawire, anayankhula zimenezi atagonja 1-0 ndipo wati oyimbira ndi yemwe anaonetsetsa kuti agonje ndithu mu masewerowa.
"Sindikufuna kuyankhula zambiri, aliyense waona momwe oyimbira achitira. Chigoli chija ndi chabwinobwino koma ziganizo za oyimbira ndi zomwe zaononga masewerowa," anatero Mkandawire.
Iye anakananso kuthilira mlomo pa momwe timuyi imakanikira kugwiritsa ntchito mipata yake ponena kuti zimachitika mu masewero.
Timu ya Red Lions yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapoints okwana asanu ndi anayi (9) pa masewero asanu ndi imodzi (6).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores