RED IKUTSOGOLERA NDANDANDA WA MPHOTO ZA OSEWERA BWINO
Timu ya Red Lions ikutsogola pa ndandanda wa matimu omwe atenga mphoto za osewera omwe asewera bwino pa masewero kochuluka kuposa timu iliyonse mu ligi ya FDH Premiership.
Timuyi yatenga mphotozi kasanu kusonyeza kuti yatenga mphotozi pa masewero aliwonse omwe asewera mu ligiyi.
Osewera awo omwe atengako mphotozi ndi Chembezi Chihoma, Matamando Matchipitsa, Henry Kamunga, Mphatso Magaleta ndi Shukuran Mussah.
Mphunzitsi watimuyi, Malumbo Mkandawire wati izi zikutanthauza kuti timuyi ilibwino mu chakachi.
"Zikungofuna kutionetsera kuti timuyi ilibwino mu chakachi komanso kuti osewera aliyense ndi wodalilika," anatero Mkandawire.
Matimu a Silver Strikers ndi Masters Security ndi omwe akubwera pachiwiri kamba koti atengako kanayi mphotozi koma Creck Sporting Club ndi Goshen City Dedza Dynamos sanatengeko mphotozi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores