RED LIONS IKUKANA KUGONJA MU LIGI
Timu ya Red Lions ikupitilira kuchitabe bwino mu ligi ya FDH Premiership pomwe yagonjetsa LUANAR Mitundu 1-0 kuti akhalabe osagonja pa bwalo la Zomba loweruka.
Timuyi inakwanitsa kupeza chigoli kudzera mwa Henry Kamunga chomwe chinawathandizira kupata mapoints onse atatu kuti afike pa nambala yachitatu mu ligiyi.
Mphunzitsi watimuyi Malumbo Mkandawire wati ndi wokondwa ndi momwe osewera ake achitira mu masewerowa.
"Mitundu sinabwere moyesa nayo imafuna kudzapambana chifukwanso tinakumana mu ligi ya NDL koma tapambana zilibwino kwambiri," anatero Mkandawire.
Iye anati kuchita bwino Kwa osewera atimuyi mu masewero omwe asewera kukuonetsa kuti timuyi ilibwino kwambiri.
Red Lions yafika pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapoints asanu ndi anayi (9) atapambana kawiri ndi kufananitsa mphamvu katatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores