NKHANI
Timu ya Masters Football Club yapeza zintchito za wotchinga pagolo wakale wa Flames, Leman Nthala, yemwe akhale mphunzitsi wa otchinga pagolo kutimuyi.
Timuyi yapanga izi pofuna kuchepetsa ntchito ya Victor Mphande yemwe amaphatikiza ntchito ziwiri ngati wothandizira mphunzitsi komanso wophunzitsa otchinga pagolowa.
Mphande, yemwe wagwira ntchito kwambiri ndi Peter Mponda, tsopano akhala ngati wothandizira chabe ndipo Nthala ndiye atenge ntchito inayo.
Malipoti ena abodza akhala akuyenda kuti Mphande wachotsedwa ntchito koma iye ali mu mzinda wa Mzuzu komwe akukalandira thandizo la mankhwala pomwe akuvutika ndi nthenda ya maso ndipo akapeza bwino akhale akubwerera kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores