Aphunzitsi atimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji ndi wachiwiri wake Harry Saidi, abwerera pa ntchito yawo ndipo ayenda ndi timuyi kumathero a sabatayi.
Awiriwa anayimitsidwa atatha masewero omwe anagonja pakhomo 3-1 ndi Kamuzu Barracks kuti akhale masewero anayi osapambanako koma tsopano abwerera.
Izi ndi malingana ndi kufufuza komanso kukambirana ndi aphunzitsiwa ndipo tsopano ali nawo paulendo wopita kumpoto kokakumana ndi Moyale Barracks ku Rumphi.
Timuyi ili pa nambala 15 ndi mapoints awiri atafananitsa masewero awiri koyenda ndi kugonja awiri apakhomo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores