SRFA, FINCA APEREKA YUNIFOLOMU NDI MIPIRA KU MATIMU
Bungwe loyendetsa ligi yakummwera kwa dziko la Southern Region Football Association ndi othandiza ligiyi a FINCA Malawi apereka yunifolomu komanso kwa matimu 16 omwe asewere mu ligi ya FINCA Premier League chaka chino.
Matimuwa alandira katunduyu pa mwambo wapadera womwe unachitikira ku mudzi wa mpira ku Chiwembe lolemba mmawa patsogolo pa kuyamba kwa ligiyi lamulungu pa 24 May 2026.
Wapampando wa bungweli, Dailes Kachala, wati ndi koyamba kuti wothandiza akapange motere ndipo wathokoza kampani ya FINCA kamba ka thandizoli.
"Tingopempha matimu kuti asungebe mwambo mu ligiyi kupewa kunyazitsa dzina la wothandizawa komanso kuwathandiza kupititsa patsogolo zomwe kampaniyi imachita," iwo anatero.
Kachala wamema anthu okhala ku Mwanza kudzakhamukira ku bwalo la Joyce Chitsulo lamulungu potsegulira ligi ya chaka chino koma wati Chikwawa United ikukayikitsa kuti isewera mu ligiyi kamba ka nkhani ya zachuma.
"Zikatero ndekuti timatenga timu yomwe inathera pa nambala yachinayi mu ligi ya mmunsi yakeyi nde chilichonse tikhale tikunena," anatero Kachala.
Ndipo mkulu woyang'ana zachuma ku kampani ya FINCA, Mada Jonas, wati kupereka kwa katunduyu akuonetsa khumbo la kampaniyi kufuna kutukula mpira kuchokera pansi penipeni.
"Tapereka katunduyu kuti matimuwa asamasowe katundu ogwiritsira ntchito mu ligi kuti chidwi chawo chizikhala popikisana pokha osati kuyang'ananso kukonza mavuto awo," anatero Jonas.
Iye wati akonza zinthu zochuluka pa tsiku lotsegulira ligi pomwe akakhale akuwadziwitsa anthu zomwe kampani yawo imapanga komanso kuti ayitana oyimba Gibo Piarson kuti akasangalatse anthu.
Ndipo woyimilira matimuwa, Isaac Tambala omwe ndi a Mchima FC yaku Thyolo yomwenso isewere mu chaka chawo choyamba mu ligi wati ndi wokondwa ndi katunduyu.
"Ifeyo takonzekera bwino ndipo poti amati mpira ndi pa bwalo koma matimu akonzekere kuti athamanga. Ife tikuyang'ana zokafika mpaka mu Supa ligi," anafo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores