Bungwe la Football Association of Malawi lasintha a zikho zamu zigawo kuti zigwirizane ndi mayina a maligi akuluakulu.
Malingana ndi uthenga womwe alemba pa tsamba lawo, maligi a Premier League amu zigawo azitchedwa Regional Division League One ndipo omwe amatchedwa kuti Division One azitchedwa Regional Division League Two ndipo a pansi pake azitchedwa District Championship.
Ndipo maligi a Premiership ndi National Division League akhalabe momwe amamvekera kuyambira kale.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores