FAM YATULUTSA NDONDOMEKO YA MPIRA WA AMAYI
Bungwe loyendetsa mpira wamiyendo mu dziko muno la Football Association of Malawi latulutsa ndondomeko yomwe itsogolere kayendetsedwe ka mpira wamiyendo wa amayi kuchokera mu chaka cha 2025 kufika mu 2027.
Izi zadziwika lolemba ku nyumba ya Mpira ku Chiwembe komwe mwambo wokhazikitsa ndondomekoyi unachitika.
Poyankhula pa mwambowu, mtsogoleri wa FAM Fleetwood Haiya anati ndondomekoyi ikuonetsa chidwi cha bungwe lawo pofuna kulimbikitsa atsikana ndi amayi komanso kupanga dziko lino kuti lipite patsogolo mu Africa.
Iye wati mpirawu ukuyenda bwino kale Koma ndondomekoyi ithandiza kupititsa patsogolo zomwe zilipo kale ku masewerowa.
"Potsata kutukula mpira wa achisodzera, kutsata dongosolo loyenera kwa akuluakulu, utsogoleri wabwino ndi maphunziro opambana a aphunzitsi zithandiza kuti osewera ambiri achisodzera atenge nawo mbali mu mpirawu," anatero Haiya.
Dongosololi lagona pa masomphenya okuti matimu a dziko lino akwanitse kugonjetsa mayik
o amu COSAFA komanso mu Africa muno.
Ndondomekoyi yagonanso pa nsanamira zisanu zomwe ndi kutukula mpira wa achisodzera, kutsata njira yoyenera mu mipikisano ndi matimu a dziko lino, za malonda ndi kufalitsa nkhani, utsogoleri wangwiro ndi maphunziro a masewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores