Anthu osiyanasiyana omwe amagulitsa mowa mu mabotolo a galasi agwidwa loweruka pa masewero omwe Ekhaya inakumana ndi Moyale Barracks pa bwalo la Mpira.
Izi ndi malingana ndi zomwe bungwe loyendetsa ligi ya FDH Premiership, a Super League of Malawi, akuletsa kupezeka kwa mabotolowa mu ma bwalo.
Mabotolowa amagwiritsidwa ntchito ngati zipangizo pa ziwawa ndi zipolowe za mmabwalomu kuchititsa kuletsa kwa mabotolowa.
Malingana ndi kafukufuku womwe tapeza, anthuwa amalowa mu mabwalowa kudzera mwa omwe amapereka chitetezo mmabwalo komanso omwe amakhala pa zipata zolowera mu ma bwalowa.
Zinthuzi izi ajambula ndi a MH photography.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores