NKHANI
Katswiri watimu ya Flames, Richard Mbulu, wachoka ku timu ya UD Songo.
Izi zadziwika loweruka pomwe timuyi imatsimikiza osewera omwe sakhala nawo mu ligi ya chaka cha 2026 ku Mozambique.
Mbulu wakhala kutimuku kwa chaka chimodzi atachokera ku Costa do Sol ndipo wakwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri mu ligi.
Iye wapambana ligi ndi chikho cha Mozambique Cup ndi timuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores