''Zoterezi nde sinnazioneko ndi Moyale'' - Mwansa
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati sanaonekonso maseweredwe oyipa omwe timu yake yaonetsa ali mphunzitsi komanso nthawi yomwe ankasewera mpira ndipo wakhumudwa kwambiri ndi kaseweredweka.
Iye amayankhula atagonja 6-0 ndi timu ya Mighty Wanderers pa bwalo la Kamuzu loweruka ndipo wati sanayembekezere kuti timu yake ikhonza kuchita moteremu.
''Ndi zokhumudwitsa kwambiri kuti tagonja moteremu chifukwa izizi nde sindinazionepo angakhake nthawi yomwe ndinkasewera mpira ndipo wochemerera athu akwiya kwambiri ndi zotsatirazi,'' anatero Mwansa.
Iye wati timu yake tsopano yataya mwayi wothera pa nambala yachinayi mu ligi komabe ayesetsa kuti achite bwino pa masewero awo otsiriza ndi Goshen City Dedza Dynamos.
Moyale ili pa nambala 8 pomwe ili ndi mapointsi 39 pa masewero 29 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores