CAF YAVOMERA FLAMES KUMENYA MADZULO
Timu ya dziko lino ikuyembekezeka kusewera masewero awo ndi Namibia madzulo kutsatira kuti bungwe la Confederation of African Football yavomera pempho lao losewera madzulo.
Bungwe la Football Association of Malawi linapempha CAF kuti masewerowa opitira ku World Cup ya 2026 aseweredwe kuyambira nthawi ya 6 koloko madzulo osati ngati mmene zimakhalira mmbuyomu ndipo avomera.
Masewerowa adzaseweredwa lachinayi momwe ndi nkati mwa sabata ndipo monga momwe wane era mkulu oona za malonda ku bungweli zithandize kuti anthu ochuluka adzaonere nawo masewerowa.
Malawi ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) mu gulu yawo pomwe Tunisia ili ndi khumi (10) kenako Namibia ili ndi asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores