"KAYA TILANDIRA CHILANGO KOMA TIPEZA ZABWINO" - KAWAYE
Mlembi wamkulu watimu ya Chitipa United, Watson Kawaye, wati timu yawo mfundo amanga kuti sakasewera ndi Civo United mawa ndipo sakuopa chilango.
Iye wayankhula izi madzulo a lachinayi ndi Yohane M'bwera wa Litala FM kuti timu yawo yapanga chiganizochi ndi cholinga chofuna chilungamo chibwere poyera.
"Kaya atichotsera mapointsi Kaya tilipira koma ganizo sitikubwenza chifukwa patsogolo pa zowawa pali zabwino. Ifeyo tikungofuna chilungamo basi." Anatero Kawaye.
Komabe ngakhale timuyi yaumitsa mtima kuti siyisewera, SULOM yaumitsanso mtima kuti masewerowa akhalakobe ndipo Chitipa ingotsatira malamulo a mpira.
Kwachema
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores