"KUTULUKA AYI KOMA MWINA TILOWA MU LIGI YAIKULU" - BANGWE ALL STARS
Timu ya Bangwe All Stars yati ilibe mantha ena aliwonse kuti mwina itha kutuluka mu NBS Bank National Division ligi pomwe yati itha kukakamizanso kuti ilowe mu ligi yaikulu.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu Davie Matemba ndi yemwe anayankhula mawuwa atagonja masewero awo achisanu mu ligi 1-0 ndi timu ya Extreme FC pa bwalo la Owen Malijani lamulungu.
Iye wati zinthudi sizikuyenda kutimu yake komabe akakamiza zinthu ndikuti masewero omwe atsala nawo akwanitse kuchita bwino.
"Tilibe mantha aliwonse ndipo sitingatuluke. Tatsala ndi masewero 15 ndekuti titapezako ma pointsi 35 ndekuti tikhoza kukakamiza ndikulowa mu ligi yaikulu," anatero Matemba.
Timuyi yapeza mapointsi awiri chabe mu ligi yaikuluyi pomwe sinapambaneko koma yangofananitsa kawiri ndi kugonja kasanu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores