"KUTAYA MAPOINTSI ANAYI SIZILI BWINO" - MPINGANJIRA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers Bob Mpinganjira wati ndi wodandaula ndi kutaya mapointsi anayi pa masewero awiri omwe asewera ponena kuti akuyenera kuti azichita bwino kwambiri mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi Goshen City Dedza Dynamos pa bwalo la Dedza lamulungu.
Iye anati timu yake inalephera kusewera momwe inakonzekerera mu chigawo choyamba koma atasintha timu yawo inayamba tsopano kusewera bwino.
"Tataya mapointsi anayi mu ligi zomwe zikuonetsa kuti sizili bwino kumbali yathu ndipo tikungoyenera kukonza cholinga zinthu zathu zikhale kuti zilibwino," anatero Mpinganjira.
Wanderers inataya mwayi woti ifike pa nambala yapamwamba mu ligiyi kamba koti yafika pa nambala yachitatu ndi mapointsi 15 pa masewero asanu ndi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores