"ZIGANIZO ZONSE TIMAPANGA NDI IFE" - SULOM
Bungwe la Super League of Malawi latsutsa kuti othandiza ligi yaikulu mdziko muno atsopano a FDH Bank sanatengepo gawo pakusankha bwalo kapena kupanga nawo ziganizo za kayendetsedwe ka ligi koma ziganizo zonse amapanga ndi iwo eni ake okhaokha.
Bungweli latulutsa kalata yofotokoza mbali yawo pa kulephereka kochititsa masewero komanso mwambo wotsegulira ligi ya chaka cha 2026-27 pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre
Bungweli lati likupepesa kwa anthu onse okonda mpira, unduna wa zamasewero, bungwe la Football Association of Malawi ndi ena onse omwe anakhudzidwa pa kuyesetsa kuti aonetsetse kufikira chimene FAM imafuna chomwe chinachititsa Kuti masewerowa asaseweredwe.
Iwo ati akuthokoza FDH Bank kamba ka chidwi chawo chofuna kuthandiza mpira mdziko muno ndipo anapereka kale K500 million yomwe ndi gawo loyamba ya K1 billion yothandizira ligiyi kwa chaka chimodzi.
Iwo atinso akukambirana ndi bankiyi pa zolakwika zomwe zinachitika ndi cho
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores