"KAYA KUMWAMBA, KAYA PANSI PA NYANJA TIKASEWERA" - WANDERERS
Timu ya Mighty Wanderers yati ndi yokonzeka kusewera masewero awo oyamba mu ligi ya FDH Premiership angakhale kuti pali mkokekoke pa kupezeka kwa bwalo la Kamuzu loweruka.
Ma bungwe a Super League of Malawi ndi Football Association of Malawi atherana mawu pa kugwiritsa ntchito bwaloli pomwe SULOM inayika masewero a timuyi pa bwaloli angakhale kuti FAM inati silili mu mulingo wabwino.
Ngakhale zili chomwechi, mmodzi mwa akuluakulu a timuyi Counsel Chancy Gondwe wati timu yako sikusokonezedwa ndi chiganizo chilichonse pa nkhaniyi.
"Ife ndi wokonzeka kukasewera kulikonse kaya ndi Zomba, kaya kumpoto kaya kumwamba kaya pansi pa nyanja," iye anatero.
Komabe Gondwe anati chomwe akudziwa ndi chakuti masewero awo ali pa bwalo la Kamuzu ndipo zinazo zangokhala ndale za mabungwe awiri.
Wanderers ikuyamba ndi kukumana ndi Karonga United pa masewero ake oyamba a ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores