Masters yapeza thandizo ku MWOS Malawi
Timu ya Masters Security yalengeza kuti yapeza thandizo kuchokera ku kampani ya Moors World of Sport (MWOS Malawi) yomwe izioneka pa zovala zawo mu ligi ya chaka chino.
Izi zadziwika lachinayi usiku pomwe timuyi imakhazikitsa ntchito za timuyi komanso kuonetsa makaka omwe azivala mu ligi ya chaka chino.
Thandizoli ndi la ndalama zokwana K200 million ndipo mgwirizano wake ndi wa chaka chimodzi ndipo utha kudzaonjezeredwa mtsogolomu.
Mmodzi mwa akuluakulu ku MWOS, Tafadzwa Matope, anati mgwirizanowu ukuonetsa chidwi cha kampani yawo pofuna kutukula mpira mdziko muno ndipo adzaonjezera ndalamazi mtsogolomu.
Ndipo wamkulu kutimu ya Masters FC, Kelvin Moyo, anati thandizoli ndi mbiri yapamwamba kwa timuyi kamba koti yangolowa kumene ndipo wati ziwathandizire kuti achite bwino mu chakachi.
Masters isewere mu chaka chake choyamba mu ligi ya chaka chino kutsatira kuti inagula malo komanso timu ya Baka City yomwe inalowanso mu ligiyi kachiwiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores